koma chokhachi anadya anyamata, ndi gawo lao la anthu amene ananka pamodzi ndi ine, Anere, Esikolo, ndi Mamure, iwo atenge gawo lao.
2 Samueli 6:1 - Buku Lopatulika Pambuyo pake Davide anamemezanso osankhika onse a mu Israele, anthu zikwi makumi atatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pambuyo pake Davide anamemezanso osankhika onse a m'Israele, anthu zikwi makumi atatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adasonkhanitsanso ankhondo okwanira 30,000, amene adaŵasankha pakati pa Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anasonkhanitsanso pamodzi ankhondo 3,000 osankhidwa pakati pa Aisraeli. |
koma chokhachi anadya anyamata, ndi gawo lao la anthu amene ananka pamodzi ndi ine, Anere, Esikolo, ndi Mamure, iwo atenge gawo lao.
Pomwepo mafuko onse a Israele anabwera kwa Davide ku Hebroni, nalankhula nati, Taonani, ife ndife fupa lanu ndi mnofu wanu.
Pamenepo Solomoni anasonkhanitsa akulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israele, kwa mfumu Solomoni mu Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova m'mzinda wa Davide, ndiwo Ziyoni.
M'mwemo Davide anamemeza Aisraele onse kuyambira Sihori wa ku Ejipito mpaka polowera ku Hamati, kutenga likasa la Mulungu ku Kiriyati-Yearimu.