Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 13:5 - Buku Lopatulika

5 M'mwemo Davide anamemeza Aisraele onse kuyambira Sihori wa ku Ejipito mpaka polowera ku Hamati, kutenga likasa la Mulungu ku Kiriyati-Yearimu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 M'mwemo Davide anamemeza Aisraele onse kuyambira Sihori wa ku Ejipito mpaka polowera ku Hamati, kutenga likasa la Mulungu ku Kiriyati-Yearimu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Choncho Davide adasonkhanitsa Aisraele onse kuyambira ku mtsinje wa Sihori ku Ejipito mpaka ku chipata cha Hamati, kuti abwere nalo Bokosi lachipangano la Mulungu kuchokera ku Kiriyati-Yearimu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Kotero Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse, kuchokera ku mtsinje wa Sihori ku Igupto mpaka ku Lebo Hamati, kuti abweretse Bokosi la Mulungu kuchokera ku Kiriati-Yearimu.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 13:5
16 Mawu Ofanana  

Pambuyo pake Davide anamemezanso osankhika onse a mu Israele, anthu zikwi makumi atatu.


Ndipo Solomoni analamulira maiko onse, kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Ejipito; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomoni masiku onse a moyo wake.


Ndipo nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israele yense pamodzi naye, msonkhano waukulu wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Ejipito, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai.


Niwakantha mfumu ya Babiloni, niwaphera ku Ribula m'dziko la Hamati. Motero anamuka nao Ayuda andende kuwachotsa m'dziko lao.


Ndipo a msonkhano onse anati kuti adzachita; pakuti chidayenera chinthuchi pamaso pa anthu onse.


Ndipo Davide ndi Aisraele onse pamodzi naye anakwera kunka ku Baala, ndiko ku Kiriyati-Yearimu wa mu Yuda, kukwera nalo kuchokera komweko likasa la Mulungu Yehova wakukhala pa akerubi, kumene aitanirako Dzina.


Ndipo Davide anasonkhanitsira Aisraele onse ku Yerusalemu, akwere nalo likasa la Yehova kumalo kwake adalikonzera.


Ndi pa nyanja zazikulu anapindula ndi mbeu za ku Sihori ndizo dzinthu za ku mtsinje; ndi kumeneko kunali msika wa amitundu.


Tsopano uli nacho chiyani m'njira ya ku Ejipito, kumwa madzi a mtsinje wa Nailo? Uli nacho chiyani m'njira ya ku Asiriya, kumwa madzi a mtsinje wa Yufurate?


Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, nafika kumizinda yao tsiku lachitatu. Koma mizinda yao ndiyo Gibiyoni, ndi Kefira, ndi Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu.


Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-Yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.


Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova.


Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikulu mu Kiriyati-Yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israele linalirira Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa