ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofooka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha;
2 Samueli 4:1 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Isiboseti mwana wa Saulo, anamva kuti Abinere adakafera ku Hebroni, manja ake anafooka, ndi Aisraele onse anavutika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Isiboseti mwana wa Saulo, anamva kuti Abinere adakafera ku Hebroni, manja ake anafooka, ndi Aisraele onse anavutika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Isiboseti, mwana wa Saulo, atamva kuti Abinere adakafera ku Hebroni, adataya mtima, ndipo Aisraele onse adachita mantha kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Isiboseti mwana wa Sauli atamva kuti Abineri waphedwa ku Hebroni, anataya mtima ndipo Aisraeli onse anachita mantha kwambiri. |
ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofooka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha;
Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.
Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka ntchito, ndipo siidzachitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.
Mfumu ya ku Babiloni yamva mbiri yao, ndipo manja ake alefuka; wagwidwa ndi nkhawa, ndi zowawa zonga za mkazi alimkudwala.
Tamva ife mbiri yake; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.