Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 6:9 - Buku Lopatulika

9 Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka ntchito, ndipo siidzachitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka ntchito, ndipo siidzachitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndidaazindikira kuti adaniwo ankangofuna kutiwopsa, namaganiza kuti, “Ayudaŵa adzachita mantha ndipo adzaleka kugwira ntchito, motero ntchitoyo siidzatha.” Koma ine ndidapemphera kuti, “Inu Mulungu, tsopano mundilimbitse mtima.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Apa adani athu onsewa ankangofuna kutiopseza. Iwo ankaganiza kuti “Tichita mantha ndi kuleka kugwira ntchito.” Tsono ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu ndilimbitseni mtima.”

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 6:9
23 Mawu Ofanana  

Koma limbikani inu, manja anu asalende; pakuti ku ntchito yanu kuli mphotho.


Ndipo anafuula ndi mau aakulu m'chinenedwe cha Ayuda kwa anthu a mu Yerusalemu okhala palinga, kuwaopsa ndi kuwavuta, kuti alande mzindawu.


Ndipo onse akuwazinga analimbitsa manja ao ndi zipangizo za siliva, ndi golide, ndi chuma, ndi zoweta, ndi zinthu za mtengo wake, pamodzi ndi nsembe zaufulu.


Mukumbukire, Mulungu wanga, Tobiya ndi Sanibalati monga mwa ntchito zao izi, ndi Nowadiya mneneri wamkazi yemwe, ndi aneneri otsala, amene anafuna kundiopsa.


Tsiku loitana ine, munandiyankha, munandilimbitsa ndi mphamvu m'moyo mwanga.


Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu.


Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu; Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake mphamvu ndi chilimbiko. Alemekezeke Mulungu.


Ndikhulupirira Inu, Yehova. Ndisachite manyazi nthawi zonse.


Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye ameme alibe mphamvu.


usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.


Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mzinda muno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.


Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lake; koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuula pamaso pake mabuulo a munthu wopyozedwa.


Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayenda m'dzina lake; ati Yehova.


Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.


kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu,


Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.


Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.


Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka;


Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.


Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa