Nehemiya 6:10 - Buku Lopatulika10 Pamenepo ndinalowa m'nyumba ya Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, wobindikizidwayo, ndipo anati, Tikomane kunyumba ya Mulungu m'kati mwa Kachisi, titsekenso pa makomo a Kachisi; pakuti akudza kudzapha iwe, inde akudza usiku kudzapha iwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Pamenepo ndinalowa m'nyumba ya Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, wobindikizidwayo, ndipo anati, Tikomane kunyumba ya Mulungu m'kati mwa Kachisi, titsekenso pa makomo a Kachisi; pakuti akudza kudzapha iwe, inde akudza usiku kudzapha iwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Nthaŵi imeneyo ndidapita ku nyumba ya Semaya, mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, amene sankatuluka m'nyumba mwake. Iye adandiwuza kuti, “Tiyeni tikabisale m'Nyumba ya Mulungu, tikatsekeko pakuti akubwera kudzakuphani. Ndithudi, akubwera usiku kudzakuphani.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Tsiku lina ndinapita ku nyumba ya Semaya mwana wa Delaya mwana wa Mehatabeli. Tsono anandiwuza kuti, “Tiyeni tikakumanire ku Nyumba ya Mulungu. Tikabisale mʼmenemo ndi kutseka zitseko chifukwa akubwera kudzakuphani. Ndithu usiku uno akubwera kudzakuphani.” Onani mutuwo |