Nehemiya 6:11 - Buku Lopatulika11 Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? Ndani wonga ine adzalowa mu Kachisi kupulumutsa moyo wake? Sindidzalowamo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? Ndani wonga ine adzalowa m'Kachisi kupulumutsa moyo wake? Sindidzalowamo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Koma ine ndidayankha kuti, “Munthu wonga ine nkuthaŵa kodi? Ndipo munthu wonga ine, kodi nkukabisala m'Nyumba ya Mulungu, kuti ndidzipulumutse? Zimenezo ai, toto, ine sindipitako!” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Koma ndinayankha kuti, “Kodi munthu ngati ine nʼkuthawa? Kapena munthu wofanana ndi ine nʼkupita ku Nyumba ya Mulungu kuti apulumutse moyo wake? Ayi, ine sindipita!” Onani mutuwo |