Ndipo Yowabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwachulukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu achione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi chinthu ichi?
2 Samueli 24:4 - Buku Lopatulika Koma mau a mfumu anapambana Yowabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yowabu ndi atsogoleri a khamulo anatuluka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma mau a mfumu anapambana Yowabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yowabu ndi atsogoleri a khamulo anatuluka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe mau a mfumu adapambana mau a Yowabu ndi a atsogoleri ankhondo aja. Choncho Yowabu ndi atsogoleri ankhondowo adachokapo kuti akaŵerenge Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu ndi atsogoleri a ankhondo. Choncho anachoka pamaso pa mfumu kupita kukawerenga anthu omenya nkhondo mu Israeli. |
Ndipo Yowabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwachulukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu achione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi chinthu ichi?
Naoloka Yordani, namanga zithando ku Aroere ku dzanja lamanja kwa mzinda uli pakati pa chigwa cha Gadi, ndi ku Yazere;
Koma mau a mfumu anamtsutsa Yowabu. Natuluka Yowabu, nakayendayenda mwa Aisraele onse, nadza ku Yerusalemu.
Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanachite monga mfumu ya Aejipito inawauza, koma analeka ana aamuna akhale ndi moyo.
Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.