Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 24:5 - Buku Lopatulika

5 Naoloka Yordani, namanga zithando ku Aroere ku dzanja lamanja kwa mzinda uli pakati pa chigwa cha Gadi, ndi ku Yazere;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Naoloka Yordani, namanga zithando ku Aroere ku dzanja lamanja kwa mudzi uli pakati pa chigwa cha Gadi, ndi ku Yazere;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Adaoloka mtsinje wa Yordani, nayambira ku Aroere, mzinda umene uli pakati pa chigwa cha ku Gadi, mpaka ku Yazere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Atawoloka Yorodani, iwo anamanga misasa yawo pafupi ndi Aroeri kummwera kwa mzinda wa ku chigwa ndipo kenaka iwo anapita ku dziko la Gadi mpaka ku Yazeri.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 24:5
12 Mawu Ofanana  

Koma mau a mfumu anapambana Yowabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yowabu ndi atsogoleri a khamulo anatuluka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israele.


Mizinda ya Aroere yasiyidwa; idzakhala ya zoweta zogona pansi, opanda woziopsa.


Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda midzi yake, napirikitsa Aamori a komweko.


Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.


Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,


Ataroti-Sofani, Yazere, ndi Yogobeha;


Kuyambira ku Aroere, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi kumudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Giliyadi, kunalibe mzinda wakutitalikira malinga ake; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.


Malire ao anayambira ku Aroere wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa ndi chidikha chonse cha ku Medeba;


Ndipo malire ao ndiwo Yazere, ndi mizinda yonse ya Giliyadi, ndi dziko la ana a Amoni logawika pakati, mpaka ku Aroere, wokhala chakuno cha Raba;


kuyambira pa Aroere, wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni;


ndi kwa iwo a ku Aroere, ndi kwa iwo a ku Sifimoti, ndi kwa iwo a ku Esitemowa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa