Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 21:4 - Buku Lopatulika

4 Koma mau a mfumu anamtsutsa Yowabu. Natuluka Yowabu, nakayendayenda mwa Aisraele onse, nadza ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Koma mau a mfumu anamlaka Yowabu. Natuluka Yowabu, nakayendayenda mwa Aisraele onse, nadza ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Koma mfumu idamkakamiza Yowabuyo. Motero Yowabu adachoka nayendera dziko lonse la Israele, pambuyo pake anabwerera ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu, kotero Yowabu anapita mu Israeli monse ndipo kenaka anabwera ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 21:4
7 Mawu Ofanana  

Nati Yowabu, Yehova aonjezere pa anthu ake monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? Nanga afuniranji chinthuchi mbuyanga, adzapalamulitsa Israele bwanji?


Ndipo Yowabu anapereka kwa Davide chiwerengo cha anthu owerengedwa. Ndipo Aisraele onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi osolola lupanga, ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri akusolola lupanga.


Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanachite monga mfumu ya Aejipito inawauza, koma analeka ana aamuna akhale ndi moyo.


Pakuti mau a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi uchita chiyani?


Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo.


Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa