Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 8:4 - Buku Lopatulika

4 Pakuti mau a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi uchita chiyani?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Pakuti mau a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi uchita chiyani?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Pajatu mau a mfumu ndi opambana. Ndani angafunse kuti, “Kodi mukuchita chiyani?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Popeza mawu a mfumu ali ndi mphamvu, ndani anganene kwa mfumuyo kuti, “Kodi mukuchita chiyani?”

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 8:4
18 Mawu Ofanana  

Koma mau a mfumu anapambana Yowabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yowabu ndi atsogoleri a khamulo anatuluka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israele.


zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israele, ndi kuti, Zoonadi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu m'malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe.


Ndipo mfumu Solomoni anatuma dzanja la Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo anamgwera, namwalira iye.


Pamenepo mfumu inalamulira Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye anatuluka namkwera, namwalira iye. Ndipo ufumu unakhazikika m'dzanja la Solomoni.


Pamenepo Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzao, popeza mfumu Dariusi adatumiza mau, anachita momwemo chofulumira.


Taona, akwatula, adzambwezetsa ndani? Adzanena naye ndani, Mulikuchita chiyani?


Ndipo mfumu ya Aejipito inaitana anamwino, ninena nao, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana aamunawo akhale ndi moyo?


Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango; koma kukoma mtima kwake kunga mame pamsipu.


Kuopsa kwa mfumu ndiko kubangula kwa mkango; womputa achimwira moyo wakewake.


tambala wolimba m'chuuno, ndi tonde, ndi mfumu yokhala ndi ankhondo ake.


Mukavomereza tsono, pakumva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, chabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu yemwe adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?


ndi okhala padziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala padziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?


Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa