Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 8:5 - Buku Lopatulika

5 Wosunga chilamulo sadzadziwa kanthu koipa; ndipo mtima wa munthu wanzeru udziwa nyengo ndi maweruzo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Wosunga chilamulo sadzadziwa kanthu koipa; ndipo mtima wa munthu wanzeru udziwa nyengo ndi maweruzo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Womvera malamulo ake sadzaona vuto lililonse. Munthu wanzeru amadziŵa nthaŵi yake ndi njira yake yochitira zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Aliyense amene amamvera lamulo lake sadzapeza vuto lililonse, ndipo munthu wanzeru amadziwa nthawi yoyenera ndi machitidwe ake.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 8:5
21 Mawu Ofanana  

Ndi a ana a Isakara, anthu akuzindikira nyengo, akudziwa zoyenera Israele kuzichita, akulu ao ndiwo mazana awiri; ndi abale ao onse anapenyerera pakamwa pao.


Pamenepo sindidzachita manyazi, pakupenyerera malamulo anu onse.


Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanachite monga mfumu ya Aejipito inawauza, koma analeka ana aamuna akhale ndi moyo.


Palibe vuto lidzagwera wolungama; koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa.


Nzeru ili pamaso pa wozindikira; koma maso a wopusa ali m'malekezero a dziko.


Wanzeru, mtima wake uli kudzanja lake lamanja; koma chitsiru, mtima wake kulamanzere.


Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.


Wanzeru maso ake ali m'mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.


Nditi, Sunga mau a mfumu, makamaka m'kulumbira Mulungu.


Efuremu azunzika, apsinjika pa mlanduwo; pakuti anafuna mwini wake kutsata lamulolo.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.


Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;


Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.


Mwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziwitso cha mzimu,


Koma chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa