Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 8:3 - Buku Lopatulika

3 Usakangaze kumchokera; usaumirire kanthu koipa; pakuti iyeyo amachita chomwe chimkonda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Usakangaze kumchokera; usaumirire kanthu koipa; pakuti iyeyo amachita chomwe chimkonda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Zinthu zikapanda kuikondweretsa mfumu, uchoke pamaso pake mwamsanga, pakuti imachita chilichonse chimene chikuikomera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Usafulumire kuchoka pamaso pa mfumu. Usawumirire chinthu choyipa, pakuti mfumu idzachita chilichonse chomwe imasangalatsidwa nacho.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 8:3
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.


Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; koma wansontho akuza utsiru.


Mwananga, opa Yehova ndi mfumu yomwe, osadudukira anthu osinthasintha.


tambala wolimba m'chuuno, ndi tonde, ndi mfumu yokhala ndi ankhondo ake.


Ngati mkulu akukwiyira, usasiye malo ako; chifukwa chifatso chipembedza utachimwa kwambiri.


Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako lili mtsempha wachitsulo, ndi mphumi yako mkuwa;


ndi okhala padziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala padziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?


ndipo chifukwa cha ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, amanenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pake; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa