Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.
2 Samueli 21:2 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu inaitana Agibiyoni, ninena nao (koma Agibiyoni, sanali a ana a Israele, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israele anawalumbirira kwa iwo, koma Saulo anafuna kuwapha mwa changu chake cha kwa ana a Israele ndi a Yuda). Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu inaitana Agibiyoni, ninena nao (koma Agibiyoni, sanali a ana a Israele, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israele anawalumbirira kwa iwo, koma Saulo anafuna kuwapha mwa changu chake cha kwa ana a Israele ndi a Yuda). Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho mfumuyo idaitana Agibiyoni. Agibiyoniwo sanali Aisraele, koma Aamori otsalira. Ngakhale Aisraele anali atalumbira kuti sadzaŵapha Agibiyoniwo, komabe Saulo adafuna kuŵaonongeratu chifukwa cha chikondi chake pa Israele ndi pa Yuda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu inayitanitsa Agibiyoni ndipo inayankhula nawo. (Tsono Agibiyoni sanali Aisraeli, koma otsala mwa Aamori. Aisraeli analumbira kuwasiya ndi moyo, koma Sauli chifukwa cha chikondi cha pa Israeli ndi Yuda, anafuna kuwawonongeratu). |
Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.
Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda.
Nati iye, Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova. M'mwemo anamuyendetsa m'galeta wake.
Koma Yehu sanasamalire kuyenda m'chilamulo cha Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wake wonse; sanaleke zoipa za Yerobowamu, zimene anachimwitsa nazo Israele.
Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.
Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.
Achita changu pa inu koma si kokoma ai, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawachitire iwowa changu.
Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawachitire chifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakuchitirani msampha.