Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 21:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mfumu inayitanitsa Agibiyoni ndipo inayankhula nawo. (Tsono Agibiyoni sanali Aisraeli, koma otsala mwa Aamori. Aisraeli analumbira kuwasiya ndi moyo, koma Sauli chifukwa cha chikondi cha pa Israeli ndi Yuda, anafuna kuwawonongeratu).

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Ndipo mfumu inaitana Agibiyoni, ninena nao (koma Agibiyoni, sanali a ana a Israele, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israele anawalumbirira kwa iwo, koma Saulo anafuna kuwapha mwa changu chake cha kwa ana a Israele ndi a Yuda).

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo mfumu inaitana Agibiyoni, ninena nao (koma Agibiyoni, sanali a ana a Israele, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israele anawalumbirira kwa iwo, koma Saulo anafuna kuwapha mwa changu chake cha kwa ana a Israele ndi a Yuda).

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Choncho mfumuyo idaitana Agibiyoni. Agibiyoniwo sanali Aisraele, koma Aamori otsalira. Ngakhale Aisraele anali atalumbira kuti sadzaŵapha Agibiyoniwo, komabe Saulo adafuna kuŵaonongeratu chifukwa cha chikondi chake pa Israele ndi pa Yuda.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 21:2
13 Mawu Ofanana  

Patapita mibado inayi, adzukulu ako adzabwereranso kuno popeza tchimo la Aamori silinafike pachimake kuti alangidwe.”


Nthawi inanso Yehova anawakwiyira Aisraeli ndipo anawutsa mtima wa Davide kuti awavutitse ndipo anati, “Pita kawerenge Aisraeli ndi Ayuda.”


Yehu anati, “Tiye kuno uwone mmene ndikudziperekera kwa Yehova.” Ndipo anayenda naye mʼgaleta mwake.


Komatu Yehu sanasamalire kusunga lamulo la Yehova Mulungu wa Israeli ndi mtima wake wonse. Iyeyo sanaleke machimo a Yeroboamu amene anachimwitsa nawo Israeli.


Ayebusi, Aamori, Agirigasi


Iwo adzakuchotsani mʼsunagoge mwawo. Kunena zoona, nthawi ikubwera imene aliyense amene adzakuphani adzaganiza kuti akutumikira Mulungu.


Popeza ndiwachitira umboni kuti ndi achangu pa zinthu za Mulungu koma osati mwachidziwitso.


Anthu amenewo akuchita changu kuti akukopeni, koma changu chawocho sichabwino. Chimene iwo akufuna ndi chakuti akuchotseni inu kwa ife, kuti mukachite changu powathandiza iwowo.


Muwononge anthu onse amene Yehova Mulungu wanu awapereka kwa inu. Musawamvere chisoni ndipo musatumikire milungu yawo pakuti umenewo udzakhala msampha kwa inu.


Sauli anati, “Mulungu andilange ngakhale kufa kumene, ngati sufa iwe Yonatani.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa