Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 10:16 - Buku Lopatulika

16 Nati iye, Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova. M'mwemo anamuyendetsa m'galeta wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Nati iye, Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova. M'mwemo anamuyendetsa m'galeta wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ndipo adamuuza kuti, “Tiye kuno, uwone m'mene ndikudziperekera kwa Chauta.” Motero adayenda naye m'galeta mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Yehu anati, “Tiye kuno uwone mmene ndikudziperekera kwa Yehova.” Ndipo anayenda naye mʼgaleta mwake.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 10:16
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Ine ndinachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele anasiya chipangano chanu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.


Nati iye, Ndachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele ataya chipangano chanu, nagumula maguwa la nsembe anu, napha aneneri anu ndi lupanga; ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.


Ndipo kudzachitika Yehu adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Hazaele; ndi Elisa adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Yehu.


Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu mu Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Eliya.


Koma Yehu sanasamalire kuyenda m'chilamulo cha Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wake wonse; sanaleke zoipa za Yerobowamu, zimene anachimwitsa nazo Israele.


Wina akutume, si m'kamwa mwako ai; mlendo, si milomo ya iwe wekha.


Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.


Pamenepo Mulungu anakomana ndi Balamu; ndipo ananena ndi iye, Ndakonza maguwa a nsembe asanu ndi awiri, ndipo ndapereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse.


Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.


Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.


Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa