Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m'dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri.
2 Samueli 20:20 - Buku Lopatulika Ndipo Yowabu anayankha nati, Iai ndi pang'ono ponse, chikhale kutali kwa ine, kuti ndingameze ndi kuononga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yowabu anayankha nati, Iai ndi pang'ono ponse, chikhale kutali kwa ine, kuti ndingameze ndi kuononga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yowabu adayankha kuti, “Iyai, ine sindikufuna konse kuwononga mzinda uno. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yowabu anayankha kuti, “Ayi ndisatero. Ine sindikufuna kuwufafaniza kapena kuwuwononga. |
Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m'dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri.
Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika mu Israele; inu mulikufuna kuononga mzinda ndi mai wa mu Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova?
Mlanduwo suli wotere ai, koma munthu wa ku dziko lamapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri, anakweza dzanja lake pa mfumu Davide; mpereke iye yekha ndipo ndidzachoka mumzinda muno. Ndipo mkaziyo anati kwa Yowabu, Onani tidzakuponyerani mutu wake kutumphitsa linga.
Nati, Ndisachite ichi ndi pang'ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa anapitawa ndi kutaya moyo wao? Chifukwa chake iye anakana kumwa. Izi anazichita ngwazi zitatuzi.