2 Samueli 20:10 - Buku Lopatulika10 Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m'dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m'dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Koma Amasa sadaachenjera nalo lupanga limene linali m'dzanja lina la Yowabu. Pomwepo Yowabuyo adamubaya nalo lupangalo m'mimba kamodzi kokha, mpaka matumbo ake kukhuthuka, naafa pomwepo. Tsono Yowabu ndi Abisai mbale wake adalondola Sheba mwana wa Bikiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Amasa sanayangʼanitsitse lupanga limene linali mʼdzanja la Yowabu, ndipo Yowabu anamubaya nalo mʼmimba ndipo matumbo ake anatuluka ndi kugwera pansi. Popanda kubayanso kachiwiri, Amasa anafa. Ndipo Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anathamangitsa Seba mwana wa Bikiri. Onani mutuwo |