Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 20:19 - Buku Lopatulika

19 Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika mu Israele; inu mulikufuna kuononga mzinda ndi mai wa mu Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika m'Israele; inu mulikufuna kuononga mudzi ndi mai wa m'Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ife ndife anthu amtendere ndi okhulupirika m'dziko la Israele. Inu mukufuna kuwononga mzinda umene uli ngati mai m'dziko la Israele. Chifukwa chiyani mukuti mufafanize choloŵa cha Chauta?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ife ndife anthu a mtendere ndi okhulupirika mu Israeli. Inu mukufuna kuwononga mzinda umene ndi mayi mu Israeli. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kufafaniza cholowa cha Yehova?”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 20:19
29 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa?


Pakuti mfumu idzamvera ndi kupulumutsa mdzakazi wake m'dzanja la munthu wakufuna kundiononga ine pamodzi ndi mwana wanga, kutichotsa ku cholowa cha Mulungu.


Chifukwa chake tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti Musagona usiku uno pa madooko a kuchipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye.


Ndipo iye analankhula, nati, Kale adanena kuti, Zoonadi adzapempha uphungu ku Abele; ndipo potero mlandu udatha.


Ndipo Yowabu anayankha nati, Iai ndi pang'ono ponse, chikhale kutali kwa ine, kuti ndingameze ndi kuononga.


Ndipo Davide ananena ndi Agibiyoni, Ndidzakuchitirani chiyani, ndipo ndidzakuyanjanitsani ndi chiyani kuti mukadalitse cholowa cha Yehova?


Popeza Inu munawapatula pa anthu onse a padziko lapansi akhale cholowa chanu, monga munanena ndi dzanja la Mose mtumiki wanu, pamene munatulutsa makolo athu mu Ejipito, Yehova Mulungu Inu.


Kuti ndione chokomacho cha osankhika anu, kuti ndikondwere nacho chikondwerero cha anthu anu, kuti ndidzitamandire pamodzi ndi cholowa chanu.


Akadatimeza amoyo, potipsera mtima wao.


Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao; mtundu womwe anausankha ukhale cholowa cha Iye yekha.


Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa, awete Yakobo, anthu ake, ndi Israele, cholowa chake.


Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwake ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine.


Ndipo Ine ndiweruza Beli mu Babiloni, ndipo ndidzatulutsa m'kamwa mwake chomwe wachimeza; ndipo amitundu sadzasonkhaniranso konse kwa iye; inde, khoma la Babiloni lidzagwa.


Adani ako onse ayasamira pa iwe, atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza; ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.


Ambuye wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni; wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake; wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake.


Ambuye wasanduka mdani, wameza Israele; wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake; nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo.


ndi dziko linayasama pakamwa pake ndi kuwameza, iwo ndi mabanja ao, ndi amuna ao onse akutsata Kora, ndi akatundu ao onse.


ndipo dziko linayasama pakamwa pake, ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, pakufa msonkhano uja; muja moto unaononga amuna mazana awiri ndi makumi asanu, nakhala iwo chizindikiro.


Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m'chigonjetso.


Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.


Pamene muyandikiza mzinda kuchita nao nkhondo, muziufuulira ndi mtendere.


Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake; Yakobo ndiye muyeso wa cholowa chake.


chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.


Midzi idalekeka mu Israele, idalekeka. Mpaka ndinauka ine Debora, ndinauka ine amai wa Israele.


Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?


Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa