Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yowabu, Abisai ndi Asahele. Ndipo Asahele anali waliwiro ngati mbawala.
2 Samueli 2:19 - Buku Lopatulika Ndipo Asahele anapirikitsa Abinere. Ndipo m'kuthamanga kwake sanapatukire kulamanja, kapena kulamanzere, pakutsata Abinere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Asahele anapirikitsa Abinere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyeyo adathamangitsa Abinere. Pothamangapo sankayang'ana uku ndi uku, maso anali pa Abinere basi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anathamangitsa Abineri ndipo sanakhotere kumanja kapena kumanzere pamene amamutsatira. |
Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yowabu, Abisai ndi Asahele. Ndipo Asahele anali waliwiro ngati mbawala.
Ndipo Abinere ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zake. Koma Asahele anakana kupatuka pakumtsata iye.
Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.
Motero Yowabu ndi Abisai mbale wake adapha Abinere, popeza iye adapha mbale wao Asahele ku Gibiyoni, kunkhondo.
Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira yonse ya Davide kholo lake, osapatukira ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.
Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipatukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako.
Koma mulimbike mtima kwambiri kusunga ndi kuchita zonse zolembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, osachipatukira kulamanja kapena kulamanzere;