Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 2:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo Abinere ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zake. Koma Asahele anakana kupatuka pakumtsata iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo Abinere ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zake. Koma Asahele anakana kupatuka pakumtsata iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Abinere adamuuza kuti, “Patukira mbali ina iliyonse, ukagwire mmodzi mwa ankhondowo, umlande zake.” Koma Asahele sadafune kuti aleke kuthamangitsa Abinere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Ndipo Abineri anati kwa iye, “Khotera kumanja kapena kumanzere: tsatira mmodzi mwa anyamatawa ndipo umulande zida zake.” Koma Asaheli sanasiye kumuthamangitsa.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 2:21
3 Mawu Ofanana  

Pomwepo Abinere anacheuka nati, Kodi ndi iwe Asahele? Iye nayankha, Ndine.


Ndipo Abinere anabwereza kunena kwa Asahele, Patuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? Ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yowabu?


Ndipo mzimu wa Yehova unamgwera Samisoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zovala zao, nawapatsa omasulira mwambiwo zovala zosinthanitsa. Koma adapsa mtima, nakwera kunka kunyumba ya atate wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa