Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 22:2 - Buku Lopatulika

2 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira yonse ya Davide kholo lake, osapatukira ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira yonse ya Davide kholo lake, osapatukira ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Iyeyo adachita zolungama pamaso pa Chauta, namatsata chitsanzo cha Davide kholo lake pa zonse, osapatukira kumanja kapena kumanzere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo anayenda mʼnjira zonse za Davide kholo lake, osatembenukira kumanja kapena kumanzere.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 22:2
18 Mawu Ofanana  

Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m'njira zanga ndi kuchita chilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga ndinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israele.


Ndipo Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova monga Davide kholo lake.


chifukwa kuti Davide adachita cholungama pamaso pa Yehova, osapatuka masiku ake onse pa zinthu zonse adamlamulira Iye, koma chokhacho chija cha Uriya Muhiti.


Ndipo Solomoni anati, Munamchitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi choonadi ndi chilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira chokoma ichi chachikulu kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wake wachifumu monga lero lino.


Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza kumisanje.


Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lake; nachita monga mwa zonse anazichita Yowasi atate wake.


Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi mu Yerusalemu; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova Mulungu wake, ngati Davide kholo lake;


Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita Davide kholo lake.


Ndipo Yehova anali ndi Yehosafati, popeza anayenda m'njira zake zoyamba za kholo lake Davide, osafuna Abaala;


Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo monse adachitira Davide kholo lake.


Momwemo anachita Hezekiya mwa Yuda lonse nachita chokoma, ndi choyenera, ndi chokhulupirika, pamaso pa Yehova Mulungu wake.


Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi atatu mphambu chimodzi.


Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.


Usapatuke kudzanja lamanja kapena kulamanzere; suntha phazi lako kusiya zoipa.


Mau a Yehova amene anadza kwa Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya, masiku a Yosiya, mwana wa Amoni mfumu ya Yuda.


Potero muzisamalira kuchita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; musamapatuka kulamanzere kapena kulamanja.


Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipatukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa