Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjezere kudandaulira kwa mfumu?
2 Samueli 19:29 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mfumu idati, “Basi ndamva usaonjezenso mau ena ai. Ine ndikufuna kuti iwe ndi Ziba mugaŵane chuma cha Saulo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu inayankha kuti, “Uneneranji zambiri? Ine ndikulamula kuti iwe ndi Ziba mugawane minda.” |
Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjezere kudandaulira kwa mfumu?
Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere kunyumba yake.
Ndipo panali mnyamata wa m'nyumba ya Saulo dzina lake Ziba; ndipo anamuitana iye afike kwa Davide; ndi mfumuyo inanena naye, Iwe ndiwe Ziba kodi? Nati iye, Ndine mnyamata wanu amene.
Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.
Pomwepo mfumu inaitana Ziba, mnyamata wa Saulo, ninena naye, Za Saulo zonse ndi za nyumba yake yonse ndampatsa mwana wa mbuye wako.
Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
koma akakhala mafunso a mau ndi maina ndi chilamulo chanu; muyang'ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi.