Mfumu niti, Ndili ndi chiyani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero chifukwa ninji?
2 Samueli 19:23 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu inanena ndi Simei, Sudzafa. Mfumu nimlumbirira iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu inanena ndi Simei, Sudzafa. Mfumu nimlumbirira iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo mfumu idauza Simei kuti, “Ndikunenetsa molumbira kuti iwe Simei suphedwa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mfumu inati kwa Simei, “Iwe Simei suphedwa.” Ndipo mfumuyo inalonjeza ndi lumbiro. |
Mfumu niti, Ndili ndi chiyani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero chifukwa ninji?
Ndipo Mefiboseti mwana wa Saulo anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasambe mapazi ake, kapena kumeta ndevu zake, kapena kutsuka zovala zake kuyambira tsiku lomuka mfumu kufikira tsiku lobwera kwao mumtendere.
Popeza tsiku lomwelo lakutuluka iwe ndi kuoloka mtsinje Kidroni, tadziwa ndithu kuti udzafadi, mwazi wako udzakhala pamutu wa iwe wekha.
Pamenepo mfumu inalamulira Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye anatuluka namkwera, namwalira iye. Ndipo ufumu unakhazikika m'dzanja la Solomoni.
Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza.
Koma Saulo anati, Sadzaphedwa lero munthu; pakuti lero Yehova anachita chipulumutso mu Israele.
Ndipo Saulo anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe chilango chidzakugwera chifukwa cha chinthu ichi.
Ndipo Davide ananena naye, Kodi udzanditsogolera kufikira ku khamulo? Nati iye, Mundilumbirire kwa Mulungu, kuti simudzandipha, kapena kundipereka m'dzanja la mbuye wanga, ndipo ndidzatsika nanu kuli khamu limene.