Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 30:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo Davide ananena naye, Kodi udzanditsogolera kufikira ku khamulo? Nati iye, Mundilumbirire kwa Mulungu, kuti simudzandipha, kapena kundipereka m'dzanja la mbuye wanga, ndipo ndidzatsika nanu kuli khamu limene.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo Davide ananena naye, Kodi udzanditsogolera kufikira ku khamulo? Nati iye, Mundilumbirire kwa Mulungu, kuti simudzandipha, kapena kundipereka m'dzanja la mbuye wanga, ndipo ndidzatsika nanu kuli khamu limene.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Davide adamufunsa kuti, “Kodi ungandiperekeze ku gulu lankhondo limenelo?” Munthuyo adati, “Muyambe mwalumbira kwa Mulungu kuti simundipha kapena kundipereka kwa mbuyanga. Mukatero ndikuperekezani ku gulu lankhondo limenelo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Davide anamupempha kuti, “Kodi unganditsogolere kumene kuli gulu lankhondoli?” Iye anayankha kuti, “Mukandilonjeza molumbira kuti simudzandipha kapena kundipereka kwa mbuye wanga, ine ndikulondolerani kumene kuli gululo.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 30:15
12 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.


ndipo inatenga wa mbumba yachifumu, nkuchita naye pangano, nkumlumbiritsa, nkuchotsa amphamvu a m'dziko;


Pali Ine, ati Ambuye Yehova, pamalo pokhala mfumu, imene idamchititsa ufumu, imene anapeputsa lumbiro lake, imene anathyola pangano lake, adzafa pamodzi ndi iye pakati pa Babiloni.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Pali Ine, lumbiro langa, analipepula, ndi pangano langa analithyola, ndidzawabweza pamutu pake.


Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakuchitirani chifundo, kuti inunso mudzachitira chifundo a m'nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa chizindikiro choona,


Ndipo Yoswa anachitirana nao mtendere napangana nao, akhale amoyo; ndi akalonga a msonkhano anawalumbirira.


Ndipo alonda anaona munthu alikutuluka m'mzinda, nanena naye, Utionetsetu polowera m'mzinda, ndipo tidzakuchitira chifundo.


Ndipo Akisi anaitana Davide, nanena naye, Pali Yehova, wakhala woongoka mtima, ndipo kutuluka kwako ndi kubwera kwako pamodzi ndi ine m'gulumo kundikomera; pakuti sindinaona choipa mwa iwe kuyambira tsiku la kufika kwako kufikira lero; koma akalongawo sakukomera mtima.


Tinathira nkhondo kumwera kwa Akereti ndi ku dziko lija la Ayuda, ndi kumwera kwa Kalebe; ndipo tinatentha mudzi wa Zikilagi ndi moto.


Ndipo pamene anatsika naye, onani, iwo anabalalika apo ponse, analinkudya, ndi kumwa, ndi kudyerera, chifukwa cha chofunkha zambiri anazitenga ku dziko la Afilisti, ndi ku dziko la Yuda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa