2 Samueli 19:24 - Buku Lopatulika24 Ndipo Mefiboseti mwana wa Saulo anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasambe mapazi ake, kapena kumeta ndevu zake, kapena kutsuka zovala zake kuyambira tsiku lomuka mfumu kufikira tsiku lobwera kwao mumtendere. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 Ndipo Mefiboseti mwana wa Saulo anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasamba mapazi ake, kapena kumeta ndevu zake, kapena kutsuka zovala zake kuyambira tsiku lomuka mfumu kufikira tsiku lobwera kwao mumtendere. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa24 Tsono Mefiboseti, mdzukulu wa Saulo, adapita kukakumana ndi mfumu. Sadasambe m'miyendo, ndevu osameta, ndipo sadachape zovala zake kuyambira tsiku limene mfumu idachoka, mpaka tsiku limene idabwerera mwamtendere. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 Mefiboseti, mdzukulu wa Sauli, nayenso anabwera kudzakumana ndi mfumu. Kuyambira tsiku limene mfumu inachoka mpaka tsiku limene inabwerera mu mtendere, iye sanasambe mapazi kaya kumeta ndevu kapena kuchapa zovala zake. Onani mutuwo |