Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 17:22 - Buku Lopatulika

Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordani. Kutacha m'mawa sanasowe mmodzi wa iwo wosaoloka Yordani.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordani. Kutacha m'mawa sanasowe mmodzi wa iwo wosaoloka Yordani.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pompo Davide adanyamukadi pamodzi ndi anthu onse amene anali naye, naoloka mtsinje wa Yordani. Pamene kunkacha, nkuti anthu onse atatha kuwoloka Yordani.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kotero Davide ndi anthu onse amene anali nawo ananyamuka ndi kuwoloka Yorodani. Pofika mmamawa, panalibe munthu amene anatsala asanawoloke Yorodani!

Onani mutuwo



2 Samueli 17:22
8 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anatuluka m'chitsime, nanka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofele anapangira zotere pa inu.


Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.


Ndipo Davide anafika ku Mahanaimu. Abisalomu naoloka Yordani, iye ndi anthu onse a Israele pamodzi naye.


Mulungu wanga, moyo wanga udziweramira m'kati mwanga; chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani, ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.


Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.


nati kwa Mose, Atumiki anu anawerenga ankhondo tinali nao, ndipo sanasowe munthu mmodzi wa ife.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


kuti akwaniridwe mau amene ati, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindinataye mmodzi.