Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati fumbi la Samariya lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.
2 Samueli 17:12 - Buku Lopatulika Chomwecho tidzamvumbulukira pamalo akuti adzapezeka, ndipo tidzamgwera monga mame agwa panthaka, ndipo sitidzasiya ndi mmodzi yense wa iye ndi anthu onse ali naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho tidamvumbulukira pa malo akuti adzapezeka, ndipo tidzamgwera monga mame agwa panthaka, ndipo sitidzasiya ndi mmodzi yense wa iye ndi anthu onse ali naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ife tidzampeza Davide kulikonse kumene adzapezeke, ndipo tidzamthira nkhondo monga m'mene mame amagwera ponseponse pa nthaka. Sipadzapulumuka ndi munthu mmodzi yemwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ife tidzapita kukamuthira nkhondo kulikonse kumene tikamupeze, ndipo ife tikamuthira nkhondo ngati mame pa nthaka. Palibe amene adzakhale wamoyo kaya iye kapena ankhondo ake. |
Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati fumbi la Samariya lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.
Mukokerane tsono ndi mbuye wanga mfumu ya Asiriya, ndipo ndidzakupatsani akavalo zikwi ziwiri, mukakhoza inu kuonetsa apakavalo.
Ndakapa, ndamwa madzi achilendo, ndi ku mapazi anga ndidzaphwetsa mitsinje yonse ya Ejipito.
Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.
Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani?
Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova ngati mvula paudzu, yosachedwera munthu, yosalindira ana a anthu.
Chifukwa chake yang'anirani, ndi kudziwa ngaka zonse alikubisalamo iye, nimubwere kwa ine ndi mau otsimikizika, pomwepo ndidzamuka nanu; ndipo akakhala m'dzikomo, ndidzampwaira pakati pa mabanja onse a Yuda.