Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzachotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa lili denene.
2 Samueli 15:14 - Buku Lopatulika Ndipo Davide ananena nao anyamata ake onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kuchoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mzinda ndi lupanga lakuthwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide ananena nao anyamata ake onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kuchoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mudzi ndi lupanga lakuthwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye Davide adauza ankhondo ake amene anali naye ku Yerusalemu kuti, “Nyamukani, tiyeni tithaŵe kuti tingasoŵe mpata wothaŵira Abisalomu. Fulumirani, kuti angatipeze mwamsanga, ndipo angatithire nkhondo ndi kutipha tonse mumzinda muno.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Davide anati kwa akuluakulu ake amene anali mu Yerusalemu. “Bwerani! Tiyeni tithawe, mwina palibe adzapulumuke kwa Abisalomu. Tiyeni tichoke msanga, mwina iye adzabwera msanga ndi kutipitirira, nʼkuwononga ife ndi mzinda wathu ndi lupanga.” |
Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzachotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa lili denene.
Ndipo anyamata a mfumu ananena kwa mfumu, Onani, monga mwa zonse mbuye wathu mfumu adzasankha, anyamata anu ndife.
Ndipo Abisalomu amene tinamdzoza mfumu yathu anafa kunkhondo. Chifukwa chake tsono mulekeranji kunena mau akuti abwere nayo mfumuyo?
Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israele analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.
Chitirani Ziyoni chokoma monga mwa kukondwera kwanu; mumange malinga a miyala a Yerusalemu.
Ndipo kalonga asatengeko cholowa cha anthu kuwazunza, ndi kulanda dziko laolao; apatse ana ake cholowa kulemba dziko lakelake, kuti anthu anga asabalalike, yense kuchoka m'dziko lake.
Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokakamizidwa, ndipo okakamirawo aukwatula ndi mphamvu.
Ndipo iwe, Kapernao, kodi udzakwezedwa kufikira Kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira ku dziko la akufa.