Abisalomu anachitira zotero Aisraele onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mlandu wao; chomwecho Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israele.
2 Samueli 15:13 - Buku Lopatulika Ndipo mthenga unafika kwa Davide nuti, Mitima ya anthu a Israele itsata Abisalomu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mthenga unafika kwa Davide nuti, Mitima ya anthu a Israele itsata Abisalomu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lina wamthenga adafika kwa Davide kudzanena kuti, “Aisraele onse ali pambuyo pa Abisalomu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munthu wina anabweretsa uthenga ndi kudzamuwuza Davide kuti, “Mitima ya Aisraeli onse ili pa Abisalomu.” |
Abisalomu anachitira zotero Aisraele onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mlandu wao; chomwecho Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israele.
Ndipo anthu onse anachisamalira, ndipo chinawakomera; zilizonse adazichita mfumu zidakomera anthu onse.
Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.
Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!
Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Khristu? Onse anati, Apachikidwe pamtanda.
Pamenepo abale a amake anamnenera mau awa onse m'makutu a eni ake onse a Sekemu; ndi mitima yao inalunjika kutsata Abimeleki; pakuti anati, Ndiye mbale wathu.