Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 12:30 - Buku Lopatulika

Nachotsa korona pamutu wa mfumu yao; kulemera kwake kunali talente wa golide; ndipo m'menemo munali miyala ya mtengo wapatali; ndipo anamuika pamutu wa Davide. Iye natulutsa zofunkha za mzindawo zambirimbiri.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Nachotsa korona pa mutu wa mfumu yao; kulemera kwake kunali talente wa golide; ndipo m'menemo munali miyala ya mtengo wapatali; ndipo anamuika pa mutu wa Davide. Iye natulutsa zofunkha za mudziwo zambirimbiri.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono Davide adaivula chisoti kumutu mfumu ya Aamoni. Chisoticho chinkalemera makilogramu agolide, ndipo pa chisotipo panali mwala wamtengowapatali. Davide adachivala chisoticho, natenga zofunkha zochuluka mumzindamo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Davide anachotsa chipewa chaufumu pamutu pa mfumu yawo ndipo Davide anavala chipewacho. Chipewacho chinkalemera makilogalamu asanu agolide, ndiponso chinali ndi miyala yokongola. Iye anatenga katundu wambiri kuchokera mu mzindawo,

Onani mutuwo



2 Samueli 12:30
4 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anasonkhanitsa anthu onse, napita ku Raba, naponyana nao, naulanda.


Ndipo Davide anatenga korona wa mfumu yao kumchotsa pamutu pake, napeza kulemera kwake talente wa golide; panalinso miyala ya mtengo wake pamenepo; ndipo anamuika pamutu pa Davide, natulutsa zankhondo za m'mzindamo zambiri ndithu.


Pakuti mufika kwa iye ndi madalitso okoma; muika korona wa golide woyengetsa pamutu pake.


ndipo utenge siliva ndi golide, nupange akorona, nuwaike pamutu pa Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe;