2 Samueli 11:17 - Buku Lopatulika Ndipo akumzindawo anatuluka, namenyana ndi Yowabu; ndipo adagwapo anthu ena, ndiwo a anyamata a Davide; ndi Uriya Muhiti anafanso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akumudziwo anatuluka, namenyana ndi Yowabu; ndipo adagwapo anthu ena, ndiwo a anyamata a Davide; ndi Uriya Muhiti anafanso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ankhondo amumzindamo adatuluka nadzamenyana ndi Yowabu. Ndipo ena mwa ankhondo a Davide adaphedwa. Uriya, Muhiti uja, nayenso adaphedwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ankhondo a mu mzindawo atabwera kudzamenyana ndi Yowabu, anthu ena a gulu la ankhondo la Davide anaphedwa ndipo Uriya Mhiti uja anaphedwanso. |
Ndani anakantha Abimeleki mwana wa Yerubeseti? Sadamponyera kodi mphero mkazi wa palinga nafa iye ku Tebezi? Munasendera bwanji pafupi potere pa lingalo? Tsono udzanena, Mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso adafa.
Chifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kuchita chimene chili choipa pamaso pake? Unakantha Uriya Muhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wake akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.
Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.