2 Samueli 11:16 - Buku Lopatulika16 Ndipo Yowabu atayang'anira mzindawo, anaika Uriya pomwe anadziwa kuti pali ngwazi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndipo Yowabu atayang'anira mudziwo, anaika Uriya pomwe anadziwa kuti pali ngwazi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Choncho pamene Yowabu ankazinga mzindawo, adaika Uriya pamalo pamene ankaŵadziŵa kuti pali ankhondo amphamvu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Kotero Yowabu atawuzinga mzindawo, anamuyika Uriya pamalo pamene amadziwa kuti pali asilikali amphamvu. Onani mutuwo |
Ndiponso udziwa chimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, inde chimene anawachitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israele, ndiwo Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lake la m'chuuno mwake, ndi pa nsapato za pa mapazi ake.