Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mzindamo. Ndipo Yowabu anabwera kuchokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.
2 Samueli 10:15 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Aaramu anaona kuti Aisraele anawathyola, anasonkhana pamodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Aaramu anaona kuti Aisraele anawathyola, anasonkhana pamodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Asiriya ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraele, adasonkanitsa ankhondo ao onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aaramu ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anasonkhananso. |
Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mzindamo. Ndipo Yowabu anabwera kuchokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.
Ndipo Hadadezere anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la chimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadadezere anawatsogolera.
Davide anakanthanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wake ku chimtsinje cha Yufurate.
nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.
Ndipo kunali, pamene Yabini mfumu ya ku Hazori anachimva, anatuma kwa Yobabu mfumu ya ku Madoni, ndi kwa mfumu ya ku Simironi, ndi kwa mfumu ya ku Akisafu,
Ndipo mafumu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israele nkhondo.