Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 10:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mzindamo. Ndipo Yowabu anabwera kuchokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mudzimo. Ndipo Yowabu anabwera kuchokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Tsono Aamoni ataona kuti Asiriya athaŵa, nawonso adathaŵa pofika Abisai, nakaloŵa mu mzinda. Apo Yowabu adaleka kumenyana ndi Aamoni, nabwerera ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai ndi kulowa mu mzinda. Nkhondo itatha, Yowabu anabwerera ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 10:14
7 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene Aaramu anaona kuti Aisraele anawathyola, anasonkhana pamodzi.


Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.


Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Sheba mwana wa Bikiri adzatichitira choipa choposa chija cha Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze mizinda ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso.


Ndinapirikitsa adani anga, ndi kuwaononga; ndiponso sindinabwerere mpaka nditawatha.


Ndipo Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, anali wamkulu wa atatuwa. Iye natukula mkondo wake pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.


za Aaramu, za Amowabu, za ana a Amoni, za Afilisti, za Amaleke, ndi zofunkha za Hadadezere, mwana wa Rehobu mfumu ya ku Zoba.


Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu mu Chigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa