Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 10:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo Hadadezere anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la chimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadadezere anawatsogolera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo Hadadezere anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la chimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadadezere anawatsogolera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Hadadezere mfumu yao adatuma amithenga kuti akabwere nawo Asiriya anzao amene anali patsidya pa mtsinje wa Yufurate. Ndipo adafika nawo ku Helamu pamodzi ndi Sobaki, mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Hadadezeri anatumiza amithenga kukayitana Aaramu amene anali ku tsidya la Mtsinje, iwo anapita ku Helamu motsogozedwa ndi Sobaki mkulu wa ankhondo a Hadadezeri.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 10:16
7 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene Aaramu anaona kuti Aisraele anawathyola, anasonkhana pamodzi.


Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisraele onse, naoloka Yordani nafika ku Helamu. Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye.


Ndipo Mulungu anamuutsira mdani wina, ndiye Rezoni mwana wa Eliyada, amene adathawa mbuye wake Hadadezere mfumu ya ku Zoba.


Ndipo Davide anakantha Hadadezere mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate.


Ndipo Aaramu a ku Damasiko anadza kudzathandiza Hadadezere mfumu ya Zoba; koma Davide anakantha Aaramu amuna zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.


Ndipo pakuona Aaramu kuti Israele anawakantha, anatumiza mithenga, natuluka nao Aaramu akukhala tsidya lija la mtsinjewo; ndi Sofaki kazembe wa khamu la Hadadezere anawatsogolera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa