2 Samueli 10:17 - Buku Lopatulika17 Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisraele onse, naoloka Yordani nafika ku Helamu. Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisraele onse, naoloka Yordani nafika ku Helamu. Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Davide atamva zimenezi, adasonkhanitsa ankhondo onse a Aisraele, naoloka mtsinje wa Yordani, nakafika ku Helamu. Apo Asiriya adandanda kuti alimbane ndi Davide, ndipo adamenyana nayedi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani ndipo anapita ku Helamu. Aaramu anayima mʼmizere yawo yankhondo kukakumana ndi Davide ndipo anamenyana naye. Onani mutuwo |