Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 10:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israele; Davide naphapo Aaramu apamagaleta mazana asanu ndi awiri, ndi apakavalo zikwi makumi anai, nakantha Sobaki kazembe wa khamu lao, nafa iye pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israele; Davide naphapo Aaramu apamagaleta mazana asanu ndi awiri, ndi apakavalo zikwi makumi anai, nakantha Sobaki kazembe wa khamu lao, nafa iye pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Koma pambuyo pake Asiriyawo adathaŵa, kuthaŵa Aisraele. Pamenepo Davide adapha anthu apa magaleta okwanira 700, ndi ankhondo okwera pa akavalo okwanira 40,000. Adamvulaza kwambiri Sobaki, mtsogoleri wa gulu lao la ankhondo uja, kotero kuti adafera pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 700 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Davide anaphanso Sobaki mtsogoleri wawo wankhondo ndipo anafera pomwepo.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 10:18
10 Mawu Ofanana  

Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisraele onse, naoloka Yordani nafika ku Helamu. Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye.


Ndipo Davide anatenga apakavalo ake chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magaleta, koma anasunga a iwo akufikira magaleta zana limodzi.


Iye nasonkhanitsa anthu, nakhala kazembe wa nkhondo, muja Davide anawapha a ku Zobawo, napita ku Damasiko, nakhala komweko, nakhala mfumu ya ku Damasiko.


Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israele; ndipo Davide anapha Aaramu apamagaleta zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi anai; napha Sofaki kazembe wa khamulo.


Ndidzawapyoza kuti sangakhoze kuuka, adzagwa pansi pa mapazi anga.


Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Muwachotse monga utsi uchotseka; monga phula lisungunuka pamoto, aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.


Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wochita ufumu ku Hazori; kazembe wake wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu.


Ndipo taonani, pomlondola Sisera Barakiyo, Yaele anatuluka kukomana naye, nati kwa iye, Idza kuno, ndidzakuonetsa munthu umfunayo. Potero anamdzera, ndipo taonani, Sisera wagwa, wafa, ndi chichiri m'litsipa mwake.


Dzanja lake analitambasulira kuchichiri, ndi dzanja lake lamanja ku nyundo ya antchito, nakhomera Sisera, nakantha mutu wake, inde, anaphwanya napyoza m'litsipa mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa