Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 10:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo pamene mafumu onse, otumikira Hadadezere, anaona kuti Aisraele anawapambana, iwo anapangana mtendere ndi Aisraele, nawatumikira. Chomwecho Aaramu anaopa kuwathandizanso ana a Amoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo pamene mafumu onse, otumikira Hadadezere, anaona kuti Aisraele anawapambana, iwo anapangana mtendere ndi Aisraele, nawatumikira. Chomwecho Aaramu anaopa kuwathandizanso ana a Amoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Tsono mafumu onse amene ankatumikira Hadadezere, ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraele, adapangana nawo za mtendere, ndipo adayamba kutumikira Aisraelewo. Motero Asiriya nawonso adaopa kumathandizanso Aamoniwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Mafumu onse amene anali pansi pa Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, iwo anachita mtendere ndi Aisraeli ndipo anakhala pansi pawo. Motero Aaramu anaopa kuthandizanso Aamoni.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 10:19
12 Mawu Ofanana  

Davide anakanthanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wake ku chimtsinje cha Yufurate.


Pamenepo Davide anaika maboma mu Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako.


Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magaleta; nakamangira Samariya misasa, naponyana nao nkhondo.


Ndipo pakuona anyamata a Hadadezere kuti Israele anawakantha, anapangana mtendere ndi Davide, namtumikira; ndi Aaramu anakana kuthandizanso ana a Amoni.


Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.


Inu mfumu ndinu mfumu ya mafumu, pakuti Mulungu wa Kumwamba anakupatsani ufumu, ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemu;


Ndipo Yoswa anabwerera m'mbuyo nthawi imeneyi nalanda Hazori nakantha mfumu yake ndi lupanga; pakuti kale Hazori unali waukulu wa maufumu aja onse.


chifukwa chakuopa chizunzo chake, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, Babiloni, mzinda wolimba! Pakuti mu ora limodzi chafika chiweruziro chanu.


Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa