2 Samueli 1:26 - Buku Lopatulika Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Yonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu aakazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Yonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu akazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mbale wanga Yonatani, ndikuvutika mu mtima chifukwa cha iwe, wakhala wapamtima wanga. Chikondi chako pa ine chinali chodabwitsa kwambiri, chinali choposa ngakhale chikondi cha akazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndikuvutika mumtima chifukwa cha iwe mʼbale wanga Yonatani, unali wokondedwa kwambiri kwa ine. Chikondi chako pa ine chinali chopambana, chopambana kuposa chikondi cha akazi. |
Koma Yonatani mwana wa Saulo anakondwera kwambiri ndi Davide. Ndipo Yonatani anauza Davide, nati, Saulo atate wanga alikufuna kukupha; chifukwa chake tsono uchenjere m'mawa, mukhale m'malo mosadziwika, nubisale;
Ndipo Yonatani anamlumbiritsa Davide kachiwiri, chifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha.
Pomwepo pochoka mnyamatayo, Davide, anauka chakumwera, nagwa nkhope yake pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.
Ndipo Yonatani mwana wa Saulo ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, namlimbitsa dzanja lake mwa Mulungu.