Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 1:26 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Ine ndikuvutika mumtima chifukwa cha iwe mʼbale wanga Yonatani, unali wokondedwa kwambiri kwa ine. Chikondi chako pa ine chinali chopambana, chopambana kuposa chikondi cha akazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

26 Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Yonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu aakazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Yonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu akazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 “Mbale wanga Yonatani, ndikuvutika mu mtima chifukwa cha iwe, wakhala wapamtima wanga. Chikondi chako pa ine chinali chodabwitsa kwambiri, chinali choposa ngakhale chikondi cha akazi.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 1:26
7 Mawu Ofanana  

“Taonani amphamvu agwa! Zida zankhondo zawonongeka!”


Pali abwenzi amene chibwenzi chawo nʼchapamaso, koma pali bwenzi limene limakukangamira kuposa mʼbale wako.


Choncho anawuza Davide kuti, “Abambo anga Sauli akufuna kukupha. Tsono uchenjere. Mmawa upite ukabisale ndipo ukakhale komweko.


Kenaka Yonatani anamulumbiritsanso Davide kuti asaleke kumukonda, pakuti ankamukonda monga ankadzikondera yekha.


Mnyamatayo anapita. Kenaka Davide anatuluka ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, nadzigwetsa pansi ndi kugunditsa nkhope yake pansi katatu. Anapsompsona nayamba kulira onse awiri, koma Davide analira kwambiri.


Ndipo Yonatani mwana wa Sauli anapita kwa Davide ku Horesi ndipo anamulimbitsa mtima pomuwuza kuti Yehova ali naye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa