Koma mnyamatayo m'mene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.
2 Akorinto 2:2 - Buku Lopatulika Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, koma iye amene ndammvetsa chisoni? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, koma iye amene ndammvetsa chisoni? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati ndine amene ndikukupweteketsani mtima, nanga ineyo adzandisangalatsa ndani, kodi si yemweyo amene ndidampweteketsa mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti ngati ndikumvetsani chisoni, kodi angandisangalatse ndani, kupatula inuyo amene ndakumvetsani chisoni? |
Koma mnyamatayo m'mene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.
Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.
monganso munativomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m'tsiku la Ambuye wathu Yesu.
Kuti ngakhale ndakumvetsani chisoni ndi kalata ija, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata ija inakumvetsani chisoni, ngakhale kwa nthawi yokha.