2 Akorinto 2:13 - Buku Lopatulika ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Masedoniya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Masedoniya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe mumtima mwanga munalibe mtendere, chifukwa sindidampeze Tito, mbale wanga. Tsono ndidatsazikana ndi anthu akumeneko nkupita ku Masedoniya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndinasowa mtendere mu mtima mwanga, chifukwa sindinapezeko mʼbale wanga Tito. Choncho ndinatsanzikana ndi anthu kumeneko nʼkupita ku Makedoniya. |
Pakuti kunakondweretsa a ku Masedoniya ndi Akaya kuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.
Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayende naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsate mapazi omwewo kodi?
Chifukwa cha ichi tatonthozedwa; ndipo m'chitonthozo chathu tinakondwera koposa ndithu pa chimwemwe cha Tito, kuti mzimu wake unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.
Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwe manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi.
Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu.
Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.
Pamenepo popita zaka khumi ndi zinai ndinakweranso kunka ku Yerusalemu pamodzi ndi Barnabasi, ndinamtenganso Tito andiperekeze.
pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya.
kwa Tito, mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.