Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 12:18 - Buku Lopatulika

18 Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayende naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsate mapazi omwewo kodi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayenda naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsata mapazi omwewo kodi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ndidapempha Tito kuti apite, kenaka ndidatuma mbale wathu wina pamodzi naye. Kodi Titoyo adakuchenjererani? Kodi suja iye ndi ine tinkachita zonse ndi mtima umodzi? Suja tinkatsata njira imodzimodzi?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ndinamupempha Tito kuti abwere kwanuko ndipo ndinamutumiza pamodzi ndi mʼbale wathu. Kodi kapena Tito anakudyerani masuku pamutu? Kodi iye ndi ine sitinachite zinthu mofanana ndi Mzimu mmodzi yemweyo?

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 12:18
13 Mawu Ofanana  

Ndipo chiyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m'dziko la Yuda; kuyambira chaka cha makumi awiri kufikira chaka cha makumi atatu mphambu ziwiri cha Arita-kisereksesi mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadye chakudya cha kazembe.


Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalande bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.


ndiponso kholo la mdulidwe wa iwo amene siali a mdulidwe okha, koma wa iwo amene atsata mayendedwe a chikhulupiriro chija cha kholo lathu Abrahamu, chimene iye anali nacho asanadulidwe.


Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwachikondi, ndi mzimu wakufatsa?


Tipatseni malo; sitinamchitire munthu chosalungama, sitinaipse munthu, sitinachenjerere munthu.


Koma Iye amene atonthoza odzichepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwake kwa Tito;


Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.


Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Khristu anamva zowawa m'malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa