Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 12:17 - Buku Lopatulika

17 Kodi wina wa iwo ndinawatuma kwa inu, ndinakuchenjererani naye kodi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Kodi wina wa iwo ndinawatuma kwa inu, ndinakuchenjererani naye kodi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Kodi kapena ndidakuchenjererani mwa aliyense amene ndidamtuma kwa inu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Kodi ndinakudyerani masuku pamutu kudzera mwa wina aliyense amene ndinamutumiza kwa inu?

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 12:17
7 Mawu Ofanana  

Koma anati, Pali Yehova, amene ndiima pamaso pake, sindidzalandira kanthu. Ndipo anamkakamiza achilandire, koma anakana.


ndipo anamva zowawa zambiri ndi asing'anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osachira pang'ono ponse, koma makamaka nthenda yake idakula,


Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine;


Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo mu Mipingo yonse.


Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayende naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsate mapazi omwewo kodi?


Chifukwa chake ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti chikhale chokonzeka chomwechi, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa