Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Akorinto 13:3 - Buku Lopatulika

popeza mufuna chitsimikizo, cha Khristu wakulankhula mwa ine; amene safooka kwa inu, koma ali wamphamvu mwa inu;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

popeza mufuna chitsimikizo, cha Khristu wakulankhula mwa ine; amene safooka kwa inu, koma ali wamphamvu mwa inu;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pamenepo mudzaona chitsimikizo chimene mukufuna chakuti Khristu amalankhula kudzera mwa ine. Iyeyu sali wofooka pa zimene amachita nanu, koma amaonetsa mphamvu zake pakati panu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

popeza mufuna chitsimikizo chakuti Khristu akuyankhula kudzera mwa ine. Iye siwofowoka pofuna kuchita nanu koma ndi wamphamvu pakati panu.

Onani mutuwo



2 Akorinto 13:3
14 Mawu Ofanana  

pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.


Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.


Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndinagiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.


Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;


(pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);


Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati pa inu, m'chipiriro chonse, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi zamphamvu.


Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti chimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndachichita chifukwa cha inu, pamaso pa Khristu;


Kwa wotereyo chilango ichi chidachitika ndi ambiri chikwanira;


Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;