kuyambira Sihori wokhala chakuno cha Ejipito mpaka malire a Ekeroni kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asikeloni, a ku Gati, ndi a ku Ekiro, ndi Avimu;
1 Samueli 6:16 - Buku Lopatulika Ndipo pamene mafumu asanu a Afilisti anaonerako, anabwerera kunka ku Ekeroni tsiku lomwelo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene mafumu asanu a Afilisti anaonerako, anabwerera kunka ku Ekeroni tsiku lomwelo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akalonga asanu a Afilisti aja ataona zimenezo, adabwerera ku Ekeroni tsiku lomwelo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atsogoleri asanu a Afilisti ataona izi anabwerera ku Ekroni tsiku lomwelo. |
kuyambira Sihori wokhala chakuno cha Ejipito mpaka malire a Ekeroni kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asikeloni, a ku Gati, ndi a ku Ekiro, ndi Avimu;
Ndipo akalonga a Afilisti anamkwerera mkaziyo, nanena naye, Umkope nuone umo muchokera mphamvu yake yaikulu, ndi umo tingakhoze kumtha khama, kuti timmange kumzunza; ndipo tidzakupatsa aliyense ndalama mazana khumi ndi limodzi.
anasiya mafumu asanu a Afilisti ndi Akanani onse, ndi Asidoni, ndi Ahivi okhala m'phiri la Lebanoni, kuyambira phiri la Baala-Heremoni mpaka polowera ku Hamati.
Chifukwa chake anatumiza likasa la Mulungu ku Ekeroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekeroni, a ku Ekeroni anafuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israele, kutipha ife ndi ana athu.
Ndipo ng'ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betesemesi, zinali kuyenda mumseu, zilikulira; sizinapatukire ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betesemesi.
Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yopalamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolide, ndi mbewa zisanu zagolide, monga mwa chiwerengo cha mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.