1 Samueli 6:15 - Buku Lopatulika15 Ndipo Alevi anatsitsa likasa la Yehova, ndi bokosi linali nalo, m'mene munali zokometsera zagolide, naziika pamwala waukuluwo; ndipo anthu a ku Betesemesi anapereka nsembe zopsereza, naphera nsembe kwa Yehova tsiku lomwelo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Ndipo Alevi anatsitsa likasa la Yehova, ndi bokosi linali nalo, m'mene munali zokometsera zagolide, naziika pa mwala waukuluwo; ndipo anthu a ku Betesemesi anapereka nsembe zopsereza, naphera nsembe kwa Yehova tsiku lomwelo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Alevi anali atatsitsa Bokosi lachipangano la Chauta ndi bokosi lina lija la pambali pake m'mene munali zinthu zagolide, naŵaika pa mwala waukuluwo. Ndipo anthu a ku Betesemesi adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina kwa Chauta pa tsiku limenelo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Alevi nʼkuti atatsitsa Bokosi la Yehova, pamodzi ndi bokosi mmene munali zinthu zagolide, ndipo anawayika pa mwala uja waukulu. Tsiku limenelo anthu a ku Beti-Semesi anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Yehova. Onani mutuwo |