1 Samueli 4:22 - Buku Lopatulika Ndipo iye anati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu lalandidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu lalandidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mau ake anali omwewo akuti, “Ulemerero wachoka kwa Aisraele poti Bokosi lachipangano la Chauta lalandidwa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ananena momwemo kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli, pakuti Bokosi la Mulungu lalandidwa.” |
Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba kukoma kwake kwa Israele; osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.
Ndipo ichi chimene chidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri.
Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.
Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake.
Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.