Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 4:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Tsono mwanayo adamutchula dzina loti Ikabodi, ndiye kuti, “Ulemerero wachoka kwa Aisraele!” Adatero chifukwa chakuti Bokosi lachipangano la Mulungu linali litalandidwa, ndiponso chifukwa cha imfa ya Eli mpongozi wake ndi ya mwamuna wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Tsono iye anatcha mwanayo dzina loti Ikabodi kutanthauza kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli,” chifukwa cha kulandidwa Bokosi la Mulungu ndi imfa ya mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 4:21
12 Mawu Ofanana  

M'mwemo anasintha ulemerero wao ndi fanizo la ng'ombe yakudya msipu.


Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu, ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.


napereka mphamvu yake mu ukapolo, ndi ulemerero wake m'dzanja la msautsi.


Ansembe ao anagwa ndi lupanga; ndipo amasiye ao sanachite maliro.


Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula.


Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba kukoma kwake kwa Israele; osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.


Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwachokera.


ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wake wa Ikabodi, mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wovala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwe kuti Yonatani wachoka.


Ndipo ichi chimene chidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri.


Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.


Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, anaphedwa.


Ndipo iye anati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu lalandidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa