1 Samueli 4:11 - Buku Lopatulika Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, anaphedwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, anaphedwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Bokosi lachipangano la Chauta lidalandidwa. Ana aŵiri aja a Eli, Hofeni ndi Finehasi, nawonso adaphedwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Bokosi la Chipangano la Yehova linalandidwa, ndiponso ana awiri Eli, Hofini ndi Finehasi anaphedwa. |
Tsoka kwa woipa! Kudzamuipira; chifukwa kuti mphotho ya manja ake idzapatsidwa kwa iye.
Koma pitani tsopano kumalo anga amene anali mu Silo, m'mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona chimene ndinachitira chifukwa cha zoipa za anthu anga Israele.
Ona, masiku alinkudza amene ndidzadula dzanja lako, ndi dzanja la nyumba ya kholo lako, kuti m'banja lako musakhalenso nkhalamba.
Ndipo udzaona masautso a mokhalamo Mulungu, m'malo mwa zabwino zonse Iye akadachitira Israele. Banja lako lidzakhala opanda nkhalamba chikhalire.
Ndipo ichi chimene chidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri.
Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.
Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake.